Tamvani mau a Yehova, amitundu inu, lalikirani m'zisumbu zakutari; ndi kuti, Iye amene anabalalitsa Israyeli adzasonkhanitsa, nadzamsunga, monga mbusa acita ndi zoweta zace.