Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova acite cotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anacotsedwa am'nsinga, kucokera ku Babulo kudza kumalo kuno.