Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.