Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yace yonse coipa conse cimene ndaunenera; cifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.