nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Comweco ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kulumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.