Kodi mwakanadi Yuda? kodi mtima wanu wanyansidwa ndi Ziyoni? bwanji mwatipanda ife, ndipo tiribe kucira? Tinayembekeza mtendere, koma sizinafike zabwino; tinayembekeza nthawi yakucira, ndipo taonani mantha!