Koma ine ndinanga mwana wa nkhosa wofatsa wotengedwa kukaphedwa; ndipo sindinadziwa kuti anandicitira ine ciwembu, kuti, Tiononge mtengo ndi zipatso zace, timdule iye pa dziko la amoyo, kuti dzina lace lisakumbukikenso.