1. NYIMBO yoposa, ndiyo ya Solomo.
2. Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwace;Pakuti cikondi cako ciposa vinyo.
3. Mafuta ako anunkhira bwino;Dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa;Cifukwa cace anamwali akukonda.
4. Undikoke; tikuthamangire;Mfumu yandilowetsa m'zipinda zace:Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe.Tidzachula cikondi cako koposa vinyo:Akukonda molungama.
5. Wakuda ine, koma wokongola,Ana akazinu a ku Yerusalemu,Ngati mahema a Kedara,Ngati nsaru zociriga za Solomo.