Ndipo mapangidwe ace a coikapo nyali ndiwo golidi wosula; kuyambira tsinde lace kufikira maluwa ace anacisula; monga mwa maonekedwe ace Yehova anaonetsa Mose, momwemo anacipanga coikapo nyali.