Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wace wa kusala kwace pa khomo la cihema cokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wace wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.