Natenge zipangizo zace zonse za utumiki, zimene atumikira nazo m'malo opatulika, nazimange m'nsaru yamadzi, ndi kuziphimba ndi cophimba ca zikopa za akatumbu, ndi kuziika paconyamulira.