Ndipo kunena za midziyo muiperekeyo yao yao ya ana a Israyeli, okhala nayo yambiri mutengeko yambiri; okhala nayo pang'ono mutengeko pang'ono; onse operekako midzi yao kwa Alevi monga mwa colowa cao adacilandira.