Ndipo ana a Israyeli ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wace; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.