Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, Popeza simunandikhulupirira Ine, kundipatula Ine pamaso pa ana a Israyeli, cifukwa cace simudzalowetsa msonkhano uwu m'dziko ndinawapatsali.