Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.