kodi muciyesa cinthu cacing'ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye, kucita nchito ya kacisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;