38. Koma Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebi mwana wa Yefune, anakhala ndi moyo mwa amuna aja adamukawo kukazonda dziko.
39. Ndipo Mose anauza ana a Israyeli mao onse awa; ndipo anthu anamva cisoni cambiri.
40. Ndipo anauka mamawa, nakwera pamwamba pa, phiri, nati, Tiri pano, tidzakwera kumka ku malo amene Yehova ananena; popeza tacimwa.
41. Ndipo Mose anati, Mutero cifukwa ninji kulakwira mau a Yehova, popeza simudzapindula nako?
42. Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.