Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena nave, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akuru makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.