Pamenepo anayenda a mbendera ya cigono ca ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lace anayang'anira Ahiyezeri mwana wa Amisadai.