Iwo ndiwo amene anawerengedwa, amene Mose anawerenga pamodzi ndi Aroni, ndi akalonga a Israyeli, ndiwo amuna khumi ndi awiri; yense kunenera nyumba ya kholo lace.