59. ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti Hazebaimu, ana a Amoni.
60. Anetini onse, ndi ana a akapolo a Solomo, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.
61. Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, ndi awa; koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao, kapena mbumba zao, ngati ali a Israyeli;
62. ana a Delaya, ana a Tobiya, ana a Nekoda, mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi anai kudza awiri.
63. Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hokozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa ndi dzina lao.