35. Ana a Harimu, mazana atatu mphambu makumi awiri.
36. Ana a Yeriko, mazana atatu mphambu makumi anai kudza asanu.
37. Ana a Lodi, Hadidi, ndi Ono, mazana asanu ndi awiri mphambu makumi awiri kudza mmodzi.
38. Ana a Senaa, zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi anai kudza makumi atatu.
39. Ansembe: ana a Yedaya, a nyumba ya Yesuwa, mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu ndi awiri kudza atatu.
40. Ana a Imeri, cikwi cimodzi mphambu makumi asanu kudza awiri.
41. Ana a Pasuru, cikwi cimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi anai ndi asanu ndi awiri.