22. Ana a Hasumu, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.
23. Ana a Bezai, mazana atatu mphambu makumi awiri kudza anai.
24. Ana a Harifi, zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
25. Ana a Gibeoni, makumi asanu ndi anai kudza asanu.
26. Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza asanu ndi atatu.
27. Amuna a ku Anatoti, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu.