Pamenepo Eliasibu mkuru wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ace ansembe, namanga cipata cankhosa; anacipatula, naika zitseko zace, inde anacipatula mpaka nsanja ya Mea, mpaka nsanja ya Hananeeli.