Ndipo akuru anthu anakhala m'Yerusalemu; anthu otsala omwe anacita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale m'Yerusalemu, mudzi wopatulika, ndi asanu ndi anai a khumi m'midzi yina.