Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! cita madyerero ako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda paceyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.