5. Kumva cidzudzulo ca anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.
6. Pakuti kuseka kwa citsiru kunga minga irikutetheka pansi pa mphika; icinso ndi cabe.
7. Indetu nsautso iyarutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.
8. Citsiriziro ca kanthu ciposa ciyambi cace; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima.
9. Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'cifuwa ca zitsiru.
10. Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano? Pakuti sulikufunsa mwanzeru pamenepo.
11. Nzeru iri yabwino pamodzi ndi colowa; akuona dzuwa apindula nayo.
12. Pakuti nzeru icinjiriza monga ndalama zicinjiriza; koma kudziwa kupambana, cifukwa nzeru isunga moyo wa eni ace.
13. Tapenya nchito ya Mulungu; pakuti ndani akhoza kulungamitsa comwe iye anacikhotetsa?
14. Tsiku la mwai kondwera, koma tsiku la tsoka lingirira; Mulungu waika ici pambali pa cinzace, kuti anthu asapeze kanthu ka m'tsogolo mwao.
15. Ndaona zonsezi masiku anga acabe; pali wolungama angofa m'cilungamo cace, ndipo pali woipa angokhalabe ndi moyo m'kuipa kwace.
16. Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha?
17. Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthawi yako isanafike?
18. Kuli kwabwino kugwira ici; indetu, usacotsepo dzanja lako pakuti yemwe aopa Mulungu adzaturuka monsemo.