Taonani, comwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi nchito zace zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wace umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lace limeneli.