Ndipo ciri conse maso anga anacifuna sindinawamana; sindinakaniza mtima wanga cimwemwe ciri conse pakuti mtima wanga unakondwera ndi nchito zanga zonse; gawo langa la m'nchito zanga zonse ndi limeneli.