16. Mwa ine akalonga ayang'anira,Ndi akuru, ngakhale oweruza onse a m'dziko,
17. Akundikonda ndiwakonda;Akundifunafuna adzandipeza.
18. Katundu ndi ulemu ziri ndi ine,Cuma cosatha ndi cilungamo.
19. Cipatso canga ciposa golidi, ngakhale golidi woyengeka;Phindu langa liposa siliva wosankhika.
20. Ndimayenda m'njira ya cilungamo,Pakati pa mayendedwe a ciweruzo,
21. Kuti ndionetse cuma akundikonda, cikhale colowa cao,Ndi kudzaza mosungira mwao.
22. Mulungu anali nane poyamba njira yace,Asanalenge zace zakale.
23. Anandiimika cikhalire ciyambire,Dziko lisanalengedwe.