16. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?
17. Ikhale ya iwe wekha,Si ya alendo okhala nawe ai.
18. Adalitsike kasupe wako;Ukondwere ndi mkazi wokula nayo.
19. Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo,Maere ace akukwanire nthawi zonse;Ukodwe ndi cikondi cace osaleka.
20. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere,Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo?