24. Woyenda ndi mbala ada moyo wace wace;Amva kulumbira, koma osaulula kanthu.
25. Kuopa anthu kuchera msampha;Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka,
26. Ambiri afunafuna ciyanjano ca mkuru;Koma ciweruzo ca munthu cicokera kwa Yehova.
27. Munthu woipa anyansa olungama;Ndipo woongoka m'njira anyansa wocimwa.