9. Wopewetsa khutu lace kuti asamve cilamulo,Ngakhale pemphero lace linyansa.
10. Wosoceretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa,Adzagwa mwini m'dzenje lace;Koma angwiro adzalandira colowa cabwino.
11. Wolemera adziyesa wanzeru;Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.
12. Posekera olungama pali ulemerero wambiri;Koma pouka oipa anthu amabisala.
13. Wobisa macimo ace sadzaona mwai;Koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.
14. Wodala munthu wakuopakosalekeza;Koma woumitsa mtima wace adzagwa m'zoipa.
15. Monga mkango wobangula ndi cirombo coyendayenda,Momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
16. Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;Koma yemwe ada cisiriro adzatanimphitsa moyo wace.
17. Woparamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;Asamuletse.
18. Woyenda mwangwiro adzapulumuka;Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.
19. Wolima munda wace zakudya zidzamkwanira;Koma wotsata anthu opanda pace umphawi udzamkwanira.