25. Wodukidwa mtima aputa makangano;Koma wokhulupirira Yehova adzakula.
26. Wokhulupirira mtima wace wace ali wopusa;Koma woyenda mwanzeru adzapulumuka,
27. Wogawira aumphawi sadzasowa;Koma wophimba maso ace adzatembereredwa kwambiri.
28. Pouka oipa anthu amabisala;Koma pakufa amenewo olungama acuruka.