1. Woipaathawapalibewomthamangitsa;Koma olungama alimba mtima ngati mkango.
2. Pocimwa dziko akalonga ace acuruka;Koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikuru.
3. Munthu waumphawi wotsendereza osaukaAkunga mvula yamadzi yokokolola dzinthu.
4. Omwe asiya cilamulo atama oipa;Koma omwe asunga cilamulo akangana nao.