10. Miyeso yosiyana, ndi malicero osiyana,Zonse ziwirizi zinyansa Yehova.
11. Ngakhale mwana adziwika ndi nchito zace;Ngati nchito yace iri yoyera ngakhale yolungama.
12. Khutu lakumva, ndi diso lopenya,Yehova anapanga onse awiriwo.
13. Usakonde tulo ungasauke;Phenyula maso, udzakhuta zakudya.
14. Wogula ati, Cacabe cimeneco.Koma atacoka adzitama.
15. Alipo golidi ndi ngale zambiri;Koma milomo yodziwa ndiyo cokometsera ca mtengo wapatari.
16. Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi wacilendo cikole umgwire mwini.
17. Zakudya za cinyengo zikondweretsa munthu;Koma pambuyo pace m'kamwa mwace mudzadzala tinsangalabwi.
18. Uphungu utsimikiza zolingalira,Ponya nkhondo utapanga upo.