1. Mwana wanzeru akondweretsa atate;Koma mwana wopusa amvetsa amace cisoni.
2. Cuma ca ucimo sicithangata:Koma cilungamo cipulumutsa kuimfa.
3. Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama;Koma amainga cifuniro ca wocimwa.
4. Wocita ndi dzanja laulesi amasauka;Koma dzanja la akhama lilemeretsa.
5. Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru;Koma wogona pakututa ndi mwana wocititsa manyazi.