10. Ndipo kudzacitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magareta ako;
11. ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse;
12. ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;
13. ndidzaononganso mafano ako osema, ndi zoimiritsa zako pakati pako; ndipo sudzalambiranso nchito za manja ako.
14. Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako.
15. Ndipo ndidzabwezera amitundu osamvera cilango mu mkwiyo waukali.