5. Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,Ndipo padirani poponderapo mapasa ace:Iye ndiye Woyera.
6. Mwa ansembe ace muli Mose ndi Aroni,Ndi Samueli mwa iwo akuitanira dzina lace;Anaitana kwa Yehova, ndipo Iye anawayankha.
7. Iye analankhula nao mumtambo woti njo:Iwo anasunga mboni zace ndi malembawa anawapatsa,
8. Munawayankha, Yehova Mulungu wathu:Munawakhalira Mulungu wakuwakhululukira,Mungakhale munabwezera cilango pa zocita zao.
9. Mkwezeni Yehova Mulungu wathu,Ndipo gwadirani pa phiri lace loyera;Pakuti Yehova Mulungu wathu ndiye woyera.