6. Kumwamba kulalikira cilungamo cace,Ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wace.
7. Onse akutumikira fano losema,Akudzitamandira nao mafano, acite manyazi:Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.
8. Ziyoni anamva nakondwera,Nasekerera ana akazi a Yuda;Cifukwa ca maweruzo anu, Yehova.
9. Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,Ndinu wokwezeka kwakukuru pamwamba pa milungu yonse yina.
10. Inuokonda Yehova, danani naco coipa:Iye asunga moyo wa okondedwa ace;Awalanditsa m'manja mwa oipa.
11. Kuunika kufesekera wolungama, Ndi cikondwerero oongoka mtima.
12. Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;Ndipo yamikani pokumbukila ciyero cace.