1. Tiyeni tiyimbire Yehova mokondwera;Tipfuule kwa thanthwe la cipulumutso cathu.
2. Tidze naco ciyamiko pamaso pace,Timpfuulire Iye mokondwera ndi masalmo.
3. Pakuti Yehova ndiye Mulungu wamkuru;Ndi mfumu yaikuru yoposa milungu yonse.
4. Malo ozama a dziko lapansi ali m'dzanja lace;Cuma ca m'mapiri comwe ndi cace.
5. Nyanja ndi yace, anailenga;Ndipo manja ace anaumba dziko louma.
6. Tiyeni, tipembedze tiwerame;Tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga:
7. Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu,Ndipo ife ndife anthu a pabusa pace, ndi nkhosa za m'dzanja mwace.Lero, mukamva mau acel
8. Musaumitse mitima yanu, ngati ku Meriba,Ngati tsiku la ku Masa m'cipululu;