2. Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu;Inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.
3. Mundicitire cifundo, Ambuye;Pakuti tsiku lonse ndiitana Inu.
4. Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu;Pakuti ndikwezera moyo wanga kwa Inu, Ambuye.
5. Pakuti fnu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira,Ndi wa cifundo cocurukira onse akuitana Inu.
6. Cherani khutu pemphero langa, Yehova;Nimumvere mau a kupemba kwanga,
7. Tsiku la msauko wanga ndidzaitana Inu;Popeza mudzandibvomereza.
8. Pakati pa milungu palibe wina wonga Inu, Ambuye;Ndipo palibe nchito zonga zanu.
9. Amitundu onse mudawalenga adzadza nadzagwada pamaso panu, Ambuye; Nadzalemekeza dzina lanu.
10. Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakucita zodabwiza;Inu ndinu Mulungu, nokhanu.
11. Mundionetse njira yanu, Yehova; ndidzayenda m'coonadi canu:Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.
12. Ndidzakuyamikani, Ambuye, Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu nthawi zonse.
13. Pakuti cifundo canu ca pa ine ncacikuru;Ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.