1. Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu,Aweruza pakati pa milungu.
2. Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti,Ndi kusamalira nkhope ya oipa?
3. Weruzani osauka ndi amasiye;Weruzani molungama ozunzika ndi osowa.
4. Pulumutsani osauka ndi aumphawi:Alanditseni m'dzanja la oipa,
5. Sadziwa, ndipo sazindikira;Amayendayenda mumdima;Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6. Ndinati Ine, Inu ndinu milungu,Ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu.
7. Komatu mudzafa monga anthu,Ndipo mudzagwa monga wina wa akulu.
8. Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi;Pakuti Inu mudzalandira amitundu onse.
Werengani mutu wathunthu Masalmo 82