4. Pakuti ici ndi colemba ca kwa Israyeli,Ciweruzo ca Mulungu wa Yakobo.
5. Anaciika cikhale mboni kwa Yosefe,Pakuturuka iye ku dziko la Aigupto:Komwe ndinamva cinenedwe cosadziwa ine.
6. Ndinamcotsera katundu paphewa pace:Manja ace anamasuka kucotengera.
7. Unaitana posautsika, ndipo ndinakulanditsa;Ndinakubvomereza mobisalika m'bingu;Ndinakuyesa ku madzi a Meriba.
8. Tamvani, anthu anga, ndidzakucitirani mboni;Israyeli, ukadzandimvera!
9. Kwanu kusakhale mulungu wafuma kwina;Nusagwadire mulungu wacilendo.
10. Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakukweza kukucotsa ku dziko la Aigupto;Yasamitsa pakamwa pako ndipo ndidzalidzaza.
11. Koma anthu anga sanamvera mau anga;Ndipo Israyeli sanandibvomera.
12. Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao,Ayende monga mwa uphungu wao wao.
13. Ha! akadandimvera anthu anga,Akadayenda m'njira zanga Israyeli!