13. Ha! akadandimvera anthu anga,Akadayenda m'njira zanga Israyeli!
14. Ndikadagonjetsa adani ao msanga,Ndikadabweza dzanja langa pa owasautsa.
15. Akumuda Yehova akadamgonjera mungakhale monyenga:Koma nyengo yao ikadakhala yosatha,
16. Akadawadyetsa naye tirigu wakometsetsa:Ndikadakukhutitsanso ndi uci wa m'thanthwe.