61. Napereka mphamvu yace m'ukapolo,Ndi ulemerero wace m'dzanja la msautsi.
62. Naperekanso anthu ace kwa lupanga;Nakwiya naco colandira cace.
63. Moto unapsereza anyamata ao;Ndi anamwali ao sanalemekezeka.
64. Ansembe ao anagwa ndi lupanga;Ndipo amasiye ao sanacita maliro.
65. Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo;Ngati ciphona cakucita nthungululu ndi vinyo.
66. Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo;Nawapereka akhale otonzeka kosatha.
67. Tero anakana hema wa Yosefe;Ndipo sanasankha pfuko la Efraimu;
68. Koma anasankha pfuko la Yuda,Phiri la Ziyoni limene analikonda.
69. Ndipo anamanga malo oyera ace ngati kaphiri,Monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha.
70. Ndipo anasankha Davide mtumiki wace,Namtenga ku makola a nkhosa:
71. Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa,Awete Yakobo, anthu ace, ndi Israyeli, colandira cace.