55. Ndipo anapitikitsa amitundu pamaso pao,Nawagawira colowa cao, ndi muyeso,Nakhalitsa mafuko a Israyeli m'mahema mwao.
56. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba,Osasunga mboni zace;
57. Koma anabwerera m'mbuyo, nacita zosakhulupirika monga makolo ao:Anapatuka ngati uta wolenda,
58. Ndipo anautsa mtima wace ndi malo amsanje ao,Namcititsa nsanje ndi mafano osema.
59. Pakumva ici Mulungu, anakwiya, Nanyozatu Israyeli;
60. Ndipo anacokera cokhalamo ca ku Silo,Cihemaco adacimanga mwa anthu;