1. Tikuyamikani Inu, Mulungu; Tiyamika, pakuti dzina lanu liri pafupi;Afotokozera zodabwiza zanu,
2. Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.
3. Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo;Ndinacirika mizati yace.
4. Ndinati kwa odzitamandira, Musamacita zodzitamandira;Ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5. Musamakwezetsa nyanga yanu;Musamalankhula ndi khosi louma.
6. Pakuti kukuzaku sikucokera kum'mawa,Kapena kumadzulo, kapena kucipululu,