8. M'kamwa mwanga mudzadzala lemekezo lanu,Ndi ulemu wanu tsiku lonse.
9. Musanditaye mu ukalamba wanga;Musandisiye, pakutha mphamvu yanga.
10. Pakuti adani anga alankhula za ine;Ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,
11. Ndi kuti, Wamsiya Mulungu:Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa,
12. Musandikhalire kutali, Mulungu;Fulumirani kundithandiza, Mulungu;
13. Adani a moyo wanga acite manyazi, nathawe;Cotonza ndi cimpepulo zikute ondifunira coipa,
14. Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,Ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.
15. Pakamwa panga padzafotokozera cilungamo canu,Ndi cipulumutso canu tsiku lonse;Pakuti sindidziwa mawerengedwe ace.