2. Ndikwatuleni m'cilungamo canu, ndi kundilanditsa:Ndicherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3. Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka;Mwalamulira kundipulumutsa;Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
4. Ndilanditseni, Mulungu wanga, m'dzanja la woipa,M'dzanja la munthu wosalungama ndi waciwawa.
5. Pakuti Inu ndinu ciyembekezo canga, Ambuye Yehova;Mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.